Chipani cha UTM chati ndichodabwa ndikuchepekedwa kwa kaganizidwe ka nduna yazachuma polephera kupeza madongosolo abwino okonzeranso chuma mdziko muno.
Kudzela muchikalata chomwe atulutsa ndipo cha sayinidwa ndi mkulu oyang’anila za chuma muchipanichi a Symon Mwayang’ana,chati mayiko ambiri amu Africa achita bwino pachuma pamene chuma chadziko lino sichikuyenda.
Chipanichi chatsindika ponena kuti ndondomeko yamkati mwachaka yomwe nduna yaza chuma yapeleka yangokhala yovomeleza kuononga ndalama za boma komanso kulimbikitsa kubwereka ndalama kudzera mwa adindo.
Comments