Akulu akulu ena ama kampani aboma monga mkulu oyang’anila kampani ya Malawi Energy Regulatory Authority a Henry Kachaje ndi mkulu wa National Oil Company of Malawi a Clement Kanyama ali mdziko la United Arab Emirates kokakambilana ndima kampani ena ogulitsa mafuta ammayiko aluya. 

 Gululi lomwe latsogozedwa ndi mlembi mu unduna wazamphamvu engineer Alfonso Chikuni, dzulo anakambilana ndi akuluakulu ena a dziko la Oman lomwe ndi limodzi mwamayiko oyenga mafuta.

 Ulendowu wadza malinga ndi malingaliro aboma ofuna kumagula mafuta munjira ya boma ndi boma (government to government).

 Mu december chaka chatha mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera analinso mdziko la United Arab Emirates kukapanganso migwirizano yonga yomweyi.

 

                    Muchinthunzi: Nthumwizi
 

Comments

Popular posts from this blog